Psalms 70

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pempho.

1Fulumirani Mulungu kundipulumutsa;
Yehova bwerani msanga kudzandithandiza.
2Iwo amene akufunafuna moyo wanga
achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa;
onse amene akukhumba chiwonongeko changa
abwezedwe mopanda ulemu.
3Onse amene akunena kwa ine kuti, “Aha, aha,”
abwerere chifukwa cha manyazi awo.
4Koma onse amene akufunafuna Inu
akondwere ndi kusangalala mwa Inu;
iwo amene amakonda chipulumutso chanu
nthawi zonse anene kuti, “Mulungu akuzike!”

5Koma ine ndine wosauka ndi wosowa;
bwerani msanga kwa ine Inu Mulungu.
Inu ndinu thandizo langa ndi momboli wanga;
Inu Yehova musachedwe.
Copyright information for NyaCCL